Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 4:7-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo ulozetse nkhope yako kuzingidwa kwace kwa Yerusalemu, ndi dzanja lako losapfundika, nuunenere.

8. Ndipo taona ndidzakumanga ndi zingwe zolimba kuti usakunkhulire, mpaka watsiriza masiku a kuzingidwa kwako.

9. Udzitengerenso tirigu, ndi barele, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi mapira, ndi mawere, nuziike m'mbale imodzi, ndi kudzipangira mkate nazo; uzidyako monga mwa kuwerenga kwa masiku udzagonawo pambali pako, ndiwo masiku mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai.

10. Ndipo cakudya cako uzicidya ciyesedwe masekeli makumi awiri tsiku limodzi; uzidyako tsiku ndi tsiku pa nthawi yace.

11. Uzimwanso madzi monga mwa muyeso, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la hini; uzimwako tsiku ndi tsiku pa nthawi yace.

12. Ndipo uzicidya ngati timikate ta barele, ndi kutioca pamaso pao ndi zonyansa za munthu.

13. Ndipo Yehova anati, Motero ana a Israyeli adz adya ca kudya cao codetsedwa, mwa amitundu kumene ndidzawaingitsirako.

14. Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! taonani, moyo wanga sunadetsedwa, pakuti ciyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye cinthu cakufa cokha, kapena cogwidwa ndi cirombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa.

15. Ndipo anati kwa ine, Taona ndakuninkha ndowe ya ng'ombe m'malo mwa zonyansa za munthu, uoce mkate wako pamenepo.

16. Nanenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndidzatyola mcirikizo, ndiwo cakudya, m'Yerusalemu; ndipo adzadya cakudyaco monga mwa muyeso, ndi mosamalira, nadzamwa madzi monga mwa muyeso, ndi kudabwa;

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 4