Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 4:15-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo anati kwa ine, Taona ndakuninkha ndowe ya ng'ombe m'malo mwa zonyansa za munthu, uoce mkate wako pamenepo.

16. Nanenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndidzatyola mcirikizo, ndiwo cakudya, m'Yerusalemu; ndipo adzadya cakudyaco monga mwa muyeso, ndi mosamalira, nadzamwa madzi monga mwa muyeso, ndi kudabwa;

17. kuti asowe cakudya ndi madzi, nasumwesumwe, naondetse mu mphulupulu zao.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 4