Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 39:21-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo ndidzaika ulemerero wanga mwa amitundu; ndi amitundu onse adzaona ciweruzo canga ndacicita, ndi dzanja langa limene ndinawaikira.

22. Ndipo nyumba ya Israyeli idzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, kuyambira tsiku ilo ndi m'tsogolomo.

23. Ndipo amitundu adzadziwa kuti nyumba ya Israyeli idalowa undende cifukwa ca mphulupulu zao, popeza anandilakwira Ine; ndipo ndinawabisira nkhope yanga; m'mwemo ndinawapereka m'dzanja la adani ao, nagwa iwo onse ndi lupanga.

24. Ndinacita nao monga mwa kudetsedwa kwao, ndi monga mwa kulakwa kwao, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.

25. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Tsopano ndidzabweza undende wa Yakobo, ndi kucitira cifundo nyumba yonse ya Israyeli, ndipo ndidzacitira dzina langa loyera nsanje.

26. Ndipo adzasenza manyazi ao, ndi zolakwa zao zonse, zimene anandilakwira nazo, pokhala mosatekeseka iwo m'dziko lao, opanda wina wakuwaopsa;

27. nditabwera nao kucoka kwa mitundu ya anthu, nditawasokolotsa m'maiko a adani ao, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa iwo pamaso pa amitundu ambiri.

28. Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, popeza ndinalola atengedwe ndende kumka kwa amitundu, koma ndinawasonkhanitsanso akhale m'dziko lao, osasiyakonso mmodzi yense wa iwowa.

29. Ndipo sindidzawabisiranso nkhope yanga, popeza ndatsanulira mzimu wanga pa nyumba ya Israyeli, ati Ambuye Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 39