Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 36:22-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Cifukwa cace nena kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Sindicicita ici cifukwa ca inu, nyumba ya Israyeli, koma cifukwa ca dzina langa loyera munaliipsalo pakati pa amitundu, kumene mudamukako.

23. Ndipo ndidzazindikiritsa dzina langa lalikuru kuti liri loyera, limene laipitsidwa mwa amitundu, limene inu munaliipsa pakati pao; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ati Ambuye Yehova, pozindikiridwa Ine woyera mwa inu pamaso pao.

24. Pakuti ndidzakutengani kukuturutsani kwa amitundu, ndi kukusokolotsani m'maiko onse, ndi kubwera nanu m'dziko lanu.

25. Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukucotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu onse.

26. Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzacotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.

27. Ndipo ndidzaika mzimu wanga m'kati mwanu, ndi kukuyendetsani m'malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwacita.

28. Ndipo mudzakhala m'dziko ndinapatsa makolo anulo, ndipo mudzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu.

29. Ndipo ndidzakupulumutsani kwa zodetsa zanu zonse, ndidzaitananso tirigu ndi kumcurukitsa, osaikiranso inu njala.

30. Ndipo ndidzacurukitsa zobala za mitengo, ndi zipatso za m'munda, kuti musalandirenso citonzo ca njala mwa amitundu.

31. Pamenepo mudzakumbukila njira zanu zoipa, ndi zocita inu zimene sizinali zabwino; ndipo mudzanyansidwa nokha pamaso panu, cifukwa ca mphulupulu zanu ndi zonyansa zanu.

32. Dziwani kuti sindicita ici cifukwa ca inu, ati Ambuye Yehova; citani manyazi, dodomani, cifukwa ca njira zanu, nyumba ya Israyeli inu.

33. Atero Ambuye Yehova, Tsiku loti ndikuyeretsani kukucotserani mphulupulu zanu zonse, ndidzakhalitsa anthu m'midzimo; ndi pamabwinja padzamangidwa.

34. Ndi dziko lacipululu lidzalimidwa, cinkana linali lacipululu pamaso pa onse opitako.

35. Ndipo adzati, Dziko ili lacipululu lasanduka ngati munda wa Edene, ndi midzi yamabwinja, ndi yacipululu, ndi yopasuka, yamangidwa malinga, muli anthu m'mwemo.

36. Pamenepo amitundu otsala pozungulira panu adzadziwa kuti Ine Yehova ndamanga malo opasuka, ndi kubzala pamene panali cipululu; Ine Yehova ndanena ndidzacita.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 36