Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 36:11-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo ndidzakucurukitsirani anthu ndi nyama; ndipo adzacuruka, nadzabalana; ndipo ndidzakhalitsa anthu pa inu, monga umo anakhalira kale, ndipo ndidzacitira inu zabwino koposa poyamba paja; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

12. Ndipo ndidzayendetsa anthu pa inu, ndiwo anthu anga Israyeli; adzakhala nawe dziko lao lao, ndipo udzakhala colowa cao osafetsanso ana ao.

13. Atero Ambuye Yehova, Popeza akuti nawe, Dzikowe ukudya anthu, nuyesa anthu ako afedwa;

14. cifukwa cace sudzadyanso anthu, kapena kuyesanso amtundu wako afedwa, ati Ambuye Yehova.

15. Ndipo sindidzakumvetsanso za manyazi a amitundu, ndipo sudzaseozanso mtonzo wa mitundu ya anthu, kapena kukhumudwitsanso anthu ako, ati Ambuye Yehova.

16. Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti,

17. Wobadwa ndi munthu iwe, muja a nyumba ya Israyeli anakhala m'dziko mwao, analidetsa ndi njira yao, ndi macitidwe ao; njira yao pamaso panga inanga cidetso ca mkazi wooloka.

18. M'mwemo ndinawatsanulira ukali wanga, cifukwa ca mwazi anautsanulira padziko, ndi cifukwa ca mafano analidetsa dziko nao;

19. ndipo ndinawabalalitsa mwa amitundu, namwazika m'maiko monga mwa njira yao; ndi monga mwa macitidwe ao ndinawaweruza.

20. Ndipo pofika iwo kwa amitundu kumene anamukako, anadetsa dzina langa loyera; popeza anthu ananena za iwowa, Awa ndi anthu a Yehova, naturuka m'dziko mwace.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 36