Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 36:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. ndipo ndidzakucurukitsirani anthu nyumba yonse ya Israyeli, yonseyi, ndi m'midzimo mudzakhala anthu, ndi kumabwinja kudzamangidwa midzi.

11. Ndipo ndidzakucurukitsirani anthu ndi nyama; ndipo adzacuruka, nadzabalana; ndipo ndidzakhalitsa anthu pa inu, monga umo anakhalira kale, ndipo ndidzacitira inu zabwino koposa poyamba paja; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

12. Ndipo ndidzayendetsa anthu pa inu, ndiwo anthu anga Israyeli; adzakhala nawe dziko lao lao, ndipo udzakhala colowa cao osafetsanso ana ao.

13. Atero Ambuye Yehova, Popeza akuti nawe, Dzikowe ukudya anthu, nuyesa anthu ako afedwa;

14. cifukwa cace sudzadyanso anthu, kapena kuyesanso amtundu wako afedwa, ati Ambuye Yehova.

15. Ndipo sindidzakumvetsanso za manyazi a amitundu, ndipo sudzaseozanso mtonzo wa mitundu ya anthu, kapena kukhumudwitsanso anthu ako, ati Ambuye Yehova.

16. Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti,

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 36