Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 36:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, unenere kwa mapiri a Israyeli, uziti, Mapiri a Israyeli inu, imvani mau a Yehova.

2. Atero Ambuye Yehova, Popeza mdani ananena za inu, Onyo, ingakhale misanje yakale iri yathu, colowa cathu;

3. cifukwa cace unenere, nuti, Atero Ambuye Yehova, Cifukwa, inde cifukwa kuti anakupasulani, nakumemezani pozungulira ponse, kuti mukhale colowa ca amitundu otsala, ndipo mwafika pa milomo ya akazitape, ndi pa mbiri yoipa ya anthu;

4. cifukwa cace, mapiri inu a Israyeli, imvani mau a Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova kunena ndi mapiri, ndi zitunda, ndi mitsinje, ndi zigwa, ndi zipululu zopasuka, ndi midzi yamabwinja, imene yakhala cakudya ndi coseketsa amitundu otsala akuzungulira;

5. cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Zoonadi pa nsanje yanga yodya nayo moto ndinanena motsutsana nao amitundu otsala, ndi Edomu lonse, amene anadzipatsira dziko langa likhale colowa cao ndi cimwemwe ca mtima wonse, ndi, mtima wopeputsa, kuti alande zace zonse zikhale zofunkha.

6. Cifukwa cace unenere za dziko la Israyeli, nuti kwa mapiri ndi kwa zitunda, kwa mitsinje ndi kwa zigwa, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndalankhula mu nsanje yanga ndi ukali wanga, popeza mwasenza manyazi a amitundu;

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 36