Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 33:9-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Koma ukacenjeza woipa za njira yace, aileke; koma iye osaileka njira yace, adzafa m'mphulupulu mwace iye, koma iwe walanditsa moyo wako.

10. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nena kwa nyumba ya Israyeli, Mumatero inu ndi kuti, Zolakwa zathu ndi zocimwa zathu zitikhalira, ndipo ticita nazo liwondewonde, tidzakhala ndi moyo bwanji?

11. Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yace, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israyeli?

12. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, unene ndi ana a anthu amtundu wako, Colungama ca wolungama sicidzamlanditsa tsiku la kulakwa kwace, ndi kunena za coipa ca woipa, sadzagwa naco tsiku lakubwerera iye kuleka coipa cace; ndi munthu wolungama sadzakhoza kukhala ndi moyo ndi cilungamo cace tsiku lakucimwa iye.

13. Ndikanena kwa wolungama kuti adzakhala ndi moyo ndithu, akatama cilungamo cace, akacita cosalungama, sizikumbukika zolungama zace ziri zonse; koma m'cosalungama cace anacicita momwemo adzafa.

14. Ndipo ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu: koma akabwerera iye kuleka cimo lace, nakacita coyenera ndi colungama;

15. woipayo akabweza cikole, nakabweza ico anacilanda mwacifwamba, nakayenda m'malemba a moyo wosacita cosalungama, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.

16. Zoipa zace ziri zonse anazicita sizidzakumbukika zimtsutse, anacita coyenera ndi colungama; adzakhala ndi moyo ndithu.

17. Koma ana a anthu a mtundu wako akuti, Njira ya Ambuye siiyenera; koma iwowa njira yao siiyenera.

18. Akabwerera wolungama kuleka cilungamo cace, nakacita cosalungama, adzafa m'mwemo.

19. Ndipo woipa akabwerera kuleka coipa cace, nakacita coyenera ndi colungama, adzakhala ndi moyo nazo.

20. Koma munati, Njira ya Ambuye siiyenera. Nyumba ya Israyeli inu, ndidzakuweruzani, yense monga mwa njira zace.

21. Ndipo kunali caka cakhumi ndi ciwiri ca undende wathu, mwezi wakhumi, tsiku lacisanu la mweziwo, anandidzera wina wopulumuka ku Yerusalemu, ndi kuti, Wakanthidwa mudzi.

22. Koma dzanja la Yehova linandikhalira madzulo, asanandifike wopulumukayo; ndipo ananditsegula pakamwa mpaka anandifika m'mawa, m'mwemo panatseguka pakamwa panga, wosakhalanso wosalankhula.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 33