Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 33:20-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Koma munati, Njira ya Ambuye siiyenera. Nyumba ya Israyeli inu, ndidzakuweruzani, yense monga mwa njira zace.

21. Ndipo kunali caka cakhumi ndi ciwiri ca undende wathu, mwezi wakhumi, tsiku lacisanu la mweziwo, anandidzera wina wopulumuka ku Yerusalemu, ndi kuti, Wakanthidwa mudzi.

22. Koma dzanja la Yehova linandikhalira madzulo, asanandifike wopulumukayo; ndipo ananditsegula pakamwa mpaka anandifika m'mawa, m'mwemo panatseguka pakamwa panga, wosakhalanso wosalankhula.

23. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

24. Wobadwa ndi munthu iwe, iwo okhala ku mabwinja a dziko la Israyeli anena, ndi kuti, Abrahamu anali yekha, nakhala nalo dziko colowa cace; koma ife ndife ambiri, dzikoli lipatsidwa kwa ife colowa cathu.

25. Cifukwa cace unene nao, Atero Ambuye Yehova, Mumadyera kumodzi ndi mwazi, mumakwezera maso anu ku mafano anu, ndi kukhetsa mwazi; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko colowa canu?

26. Mumatama lupanga lanu, mumacita conyansa, mumaipsa yense mkazi wa mnansi wace; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko colowa canu?

27. Uzitero nao, Atero Ambuye Yehova, Pali Ine, iwo okhala kumabwinja adzagwadi ndi lupanga, ndi iye ali kuthengo koyera ndidzampereka kwa zirombo, adyedwe nazo; ndi iwo okhala m'malinga ndi m'mapanga adzafa ndi mliri.

28. Ndipo ndidzasanduliza dziko likhale lacipululu ndi lodabwitsa, ndi mphamvu yace yodzikuza idzatha, ndi mapiri a Israyeli adzakhala acipululu, osapitako munthu.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 33