Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 32:8-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndidzakudetsera miyuni ronse yakuunikira kuthambo, ndi kucititsa mdima pa dziko lako, ati Ambuye Yehova.

9. Ndidzabvutanso mitima ya mitundu yambiri ya anthu, pakufikitsa Ine cionongeko cako mwa amitundu, m'maiko amene sunawadziwa.

10. Ndipo ndidzasumwitsa nawe mitundu yambiri ya anthu, ndi mafumu ao adzacita malunga cifukwa ca iwe, pakung'animitsa Ine lupanga langa pamaso pao; ndipo adzanjenjemera mphindi zonse, yense cifukwa ca moyo wace tsiku lakugwa Iwe,

11. Pakuti atero Ambuye Yehova, Lupanga la mfumu ya ku Babulo lidzakudzera.

12. Ndidzagwetsa aunyinji ako ndi malupanga a eni mphamvu, ndiwo onse oopsetsa a amitundu; ndipo adzaipsa kudzikuza kwa Aigupto, ndi aunyinji ace onse adzaonongeka.

13. Ndidzaononganso nyama zace zonse za ku madzi ambiri; ndi phazi la munthu silidzabvundulira, ndi ziboda za nyama zosawabvundulira.

14. Pamenepo ndidzadikhitsa madzi ace, ndi kuyendetsa madzi a m'mitsinje mwao ngati mafuta, ati Ambuye Yehova.

15. Pakusanduliza Ine dziko la Aigupto likhale lopasuka ndi labwinja, dziko losowa zodzaza zace, pakukantha Ine onse okhala m'mwemo, pamenepo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.

16. Iyi ndi nyimbo ya maliro adzalira nayo, ana akazi a amitundu adzacita nayo maliro; adzalirira nayo Aigupto ndi aunyinji ace onse, ati Ambuye Yehova.

17. Kunalinso caka cakhumi ndi ciwiri, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi, anandidzera mau a Yehova, ndi kuti,

18. Wobadwa ndi munthu iwe, lirira aunyinji a Aigupto, nuwagwetsere iye ndi ana akazi a amitundu omveka kunsi kwa dziko, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 32