Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 31:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali caka cakhumi ndi cimodzi, mwezi wacitatu, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, nena kwa Farao mfumu ya Aigupto ndi aunyinji ace, Ufanana ndi yani m'ukulu wako?

3. Taona, Asuri anali mkungudza wa ku Lebano ndi nthambi zokoma zobvalira, wautali msinkhu, kunsonga kwace ndi kumitambo.

4. Madzi anaumeretsa, cigumula cinaukulitsa, mitsinje yace inayenda, nizungulira munda wace, nipititsa micera yace ku mitengo yonse ya kuthengoko.

5. Cifukwa cace msinkhu wace unaposa mitengo yonse ya kuthengo, ndi nthambi zace zinacuruka, ndi nthawi zace zinatalika, Cifukwa ca madzi ambiri pophuka uwu.

6. Mbalame zonse za m'mlengalenga zinamanga zisa zao pa nthambi zace, ndi pansi pa nthawi zace zinaswana nyama zonse za kuthengo, ndi pa mthunzi wace inakhala mitundu yonse yaikuru ya anthu.

7. M'mwemo unakoma m'ukulu wace, m'kutalika kwa nthawi zace, popeza muzu wace unakhala ku madzi ambiri.

8. Mikungudza ya m'munda wa Mulungu siinathe kuubisa, milombwasimanga nthambi zace, mifula siinanga nthawi zace; m'munda wa Mulungu munalibe mtengo wofanana nao kukoma kwace.

9. Ndinaupanga wokoma ndi nthawi zace zocuruka; ndi mitengo yonse ya m'Edene inali m'munda wa Mulungu inacita nao nsanje.

10. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mtengowo unakuza msinkhu wace, nufikitsa nsonga yace kumitambo, nukwezeka mtima wace m'kukula kwace,

11. ndidzaupereka m'dzanja la wamphamvu wa amitundu; iye adzacita naotu, Ine ndautaya mwa coipa cace.

12. Ndipo alendo oopsawo a amitundu anaulikhatu, nausiya; nthawi zace zidagwa pamapiri ndi m'zigwa zonse, ndi nthambi zace zinatyokera ku timitsinje tonse ta m'dziko; ndi mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi inatsika ku mthunzi wace, niusiya.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 31