Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona, Ine ndilimbana naye Parao mfumu ya Aigupto, ndidzatyola manja ace, lolimba ndi lotyokalo, ndi kutayitsa lupanga m'dzanja lace.