Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 30:15-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo ndidzatsanulira ukali wanga pa Sini, polimbika peni peni pa Aigupto, ndi kulikha aunyinji a No.

16. Ndipo ndidzaika moto m'Aigupto; Sini adzamva kuwawa kwakukuru, ndi No adzagawika pakati, ndi Nofu adzaona adani usana.

17. Anyamata a Avene ndi Pibezeti adzagwa ndi lupanga, ndi midziyi idzalowa undende.

18. Ndi ku Tehafinehesi kudzada usana, pakutyola Ine magoli a Aigupto komweko; ndi mphamvu yace yodzikuza idzalekeka m'menemo; kunena za ilo mtambo udzaliphimba, ndi ana ace akazi adzalowa undende.

19. Motero ndidzakwaniritsa maweruzo m'Aigupto, ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

20. Ndipo kunali caka cakhumi ndi cimodzi, mwezi woyamba, tsiku lacisanu ndi ciwiri la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

21. Wabadwa ndi munthu iwe, ndatyola dzanja la Parao mfumu ya Aigupto, ndipo taona, silinamangidwa kuti lipole, kulikulunga ndi nsaru, kulilimbitsa ligwire lupanga.

22. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona, Ine ndilimbana naye Parao mfumu ya Aigupto, ndidzatyola manja ace, lolimba ndi lotyokalo, ndi kutayitsa lupanga m'dzanja lace.

23. Ndipo ndidzamwaza Aaigupto mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.

24. Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babulo, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lace; koma ndidzatyola manja a Parao, ndipo adzabuula pamaso pace mabuulo a munthu wopyozedwa.

25. Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babulo, koma manja a Parao adzagwa; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakuika Ine lupanga langa m'dzanja la mfumu ya ku Babulo, nalitambasula Iye pa dziko la Aigupto.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 30