Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 30:13-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Atero Ambuye Yehova, Ndidzaononganso mafano, ndi kuleketsa milungu yopanda pace ku Nofu; ndipo sadzaonekanso kalonga wocokera ku Aigupto, ndipo ndidzaopsa dziko la Aigupto.

14. Ndipo ndidzasandutsa Patro labwinja, ndi kuika moto m'Zoani, ndi kukwaniritsa maweruzo m'No.

15. Ndipo ndidzatsanulira ukali wanga pa Sini, polimbika peni peni pa Aigupto, ndi kulikha aunyinji a No.

16. Ndipo ndidzaika moto m'Aigupto; Sini adzamva kuwawa kwakukuru, ndi No adzagawika pakati, ndi Nofu adzaona adani usana.

17. Anyamata a Avene ndi Pibezeti adzagwa ndi lupanga, ndi midziyi idzalowa undende.

18. Ndi ku Tehafinehesi kudzada usana, pakutyola Ine magoli a Aigupto komweko; ndi mphamvu yace yodzikuza idzalekeka m'menemo; kunena za ilo mtambo udzaliphimba, ndi ana ace akazi adzalowa undende.

19. Motero ndidzakwaniritsa maweruzo m'Aigupto, ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

20. Ndipo kunali caka cakhumi ndi cimodzi, mwezi woyamba, tsiku lacisanu ndi ciwiri la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

21. Wabadwa ndi munthu iwe, ndatyola dzanja la Parao mfumu ya Aigupto, ndipo taona, silinamangidwa kuti lipole, kulikulunga ndi nsaru, kulilimbitsa ligwire lupanga.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 30