Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 29:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo ndidzasandutsa dziko la Aigupto labwinja pakati pa maiko a mabwinja; ndi midzi yace pakati pa midzi yopasuka idzakhala yabwinja zaka makumi anai; ndipo ndidzamwaza Aaigupto mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.

13. Pakuti atero Ambuye Yehova, Zitatha zaka makumi anai ndidzasonkhanitsa Aaigupto ku mitundu ya anthu kumene anamwazikirako;

14. ndipo ndidzabweza undende wa Aigupto, ndi kuwabwezera ku dziko la Patro, ku dziko la kubadwa kwao, ndi komweko adzakhala ufumu wopepuka,

15. Udzakhala wopepuka wa maufumu onse, sudzadzikwezanso pa amitundu; ndipo ndidzawacepsa, kuti asacitenso ufumu pa amitundu.

16. Ndipo sudzakhalanso cotama ca nyumba ya Israyeli, kukumbutsa mphulupulu, pakuwatembenukira kuwatsata; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

17. Ndipo kunali caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

18. Wobadwa ndi munthu iwe, Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anacititsa ankhondo ace nchito yaikuru yoponyana ndi Turo; mitu yonse inacita dazi, ndi mapewa onse ananyuka; koma analibe kulandira mphotho ya ku Turo, iye kapena ankhondo ace, pa nchito anagwirayo;

19. cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzapereka dziko la Aigupto kwa Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo; ndipo adzacoka nao aunyinji ace, nadzafunkha ndi kulanda zace, ndizo mphotho ya khamu lace.

20. Ndamninkha dziko la Aigupto combwezera nchito yace, popeza anandigwirira nchito, ati Ambuye Yehova.

21. Tsiku ilo ndidzameretsera nyumba ya Israyeli nyanga; ndipo ndidzakutsegulira pakamwa pakati pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 29