Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 29:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka cakhumi, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi ndi ciwiri la mweziwo, anandidzera mau a Yehova, akuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa: nkhope yako itsutsane naye Farao mfumu ya Aigupto, nunenere motsutsana ndi iye, ndi Aigupto lonse;

3. nena, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona nditsutsana nawe, Farao mfumu ya Aigupto, ng'ona yaikuru yakugona m'kati mwa mitsinje yace, imene ikuti, Mtsinje wanga ndi wangatu, ndadzipangira ndekha uwu.

4. Koma ndidzaika mbedza m'kamwa mwako, ndi kumamatiritsa nsomba za m'mitsinje mwako ku mamba ako; ndipo ndidzakukweza kukuturutsa m'kati mwa mitsinje yako, pamodzi ndi nsomba zonse za m'mitsinje mwako zomamatira pa mamba ako.

5. Ndipo ndidzakutaya kucipululu, iwe ndi nsomba zonse za m'mitsinje mwako; udzagwa kuthengo koyera, sudzaunjikidwa, kapena kuoledwa; ndakupereka ukhale cakudya ca zirombo za padziko, ndi mbalame za kumlengalenga,

6. Ndi onse okhala m'Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, popeza anakhalira nyumba ya Israyeli mcirikizo wabango.

7. Muja anakugwira ndi dzanja unatyoka, ndi kulasa mapewa ao onse; ndi muja anakutsamira unatyoka, ndi kuwagwedeza ziuno zao zonse.

8. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona, ndikudzera ndi lupanga, ndi kukulikhira munthu ndi nyama.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 29