Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 27:18-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Damasiko anagulana nawe malonda cifukwa ca zambirizo udazipanga, cifukwa ca kucuruka kwa cuma ciri conse, ndi vinyo wa ku Keliboni, ndi ubweya wa nkhosa woyera.

19. Vedani ndi Yavani anagula malonda ako ndi thonje, unagulana nao citsulo cosalala, ngaho, ndi mzimbe.

20. Dedani anagulana nawe malonda ndi nsaru za mtengo wace zoyenda nazo pa kavalo.

21. Arabu ndi akalonga onse a ku Kedara anazolowerana nao malonda ako; ana a nkhosa, nkhosa zamphongo, ndi mbuzi, izi anagulana nawe.

22. Amalonda a ku Seba ndi a ku Rama anagulana nawe malonda; anagula malonda ako ndi zonunkhira zoposa ziri zonse, ndi miyala iri yonse ya mtengo wace, ndi golidi.

23. Harani ndi Kane ndi Edene, amalonda a ku Seba Asuri ndi Kilimadi, anagulana nawe malonda.

24. Awa anagulana nawe malonda ndi zobvala zosankhika, ndi mitumba ya nsaru zofiirira ndi zopikapika, ndi cuma ca thonje lopotapota, ndi zingwe zopota zolimba za malonda ako.

25. Zombo za ku Tarisi ndizo amtengatenga a malonda ako; ndipo unadzazidwa ndi cuma ndi ulemu waukuru pakati pa nyanja,

26. Opalasa ako anakufikitsa ku madzi akuru; mphepo ya kum'mawa inakutyola m'kati mwa nyanja,

27. Cuma cako, zako zogulana nazo malonda ako, amarinyero ako, ndi oongolera ako, amisiri ako, ndi ogulitsa malonda ako, ndi ankhondo ako onse okhala mwa iwe, pamodzi ndi msonkhano wonse uli pakati pa iwe, adzagwa m'kati mwa nyanja tsiku la kugwa kwako.

28. Pakumveka mpfuu wa oongolera ako mabwalo ako adzagwedezeka.

29. Ndi onse ogwira nkhafi, amarinyero, ndi oongolera onse a kunyanja, adzatsika ku zombo zao, nadzaima pamtunda,

30. nadzamveketsa mau ao pa iwe, nadzalira mowawa mtima, nadzathira pfumbi pamitu pao, nadzakunkhulira m'maphulusa,

31. nadzameta mpala, cifukwa ca iwe, nadzadzimangira ziguduli m'cuuno, nadzakulirira ndi mtima wowawa maliro owawa.

32. Ndipo pakulira adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kukulirira, ndi kuti, Wakunga Turo ndani, wakunga uyu waonongeka pakati pa nyanja?

33. Pakuturuka malonda ako m'nyanja unadzaza mitundu yambiri ya anthu, unalemeretsa mafumu a pa dziko lapansi ndi cuma cako cocuruka ndi malonda ako.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 27