Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 26:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo adzalanda cuma cako ndi kufunkha malonda ako, nadzagwetsa malinga ako ndi kupasula nyumba zako zofunika, nadzaponya miyala yako, ndi mitengo yako, ndi pfumbi lako, m'madzi.

13. Ndipo ndidzaleketsa phokoso la nyimbo zako, ndi kulira kwa mazeze ako sikudzamvekanso.

14. Ndipo ndidzakuyesa pathanthwe poyera; udzakhala poyanika khoka, sadzakumanganso; pakuti Ine Yehova ndacinena, ati Ambuye Yehova.

15. Atero Ambuye Yehova kwa Turo, Zisumbu sizidzagwedezeka nanga pomveka kugwa kwako, pabuula olasidwa, pakucitika kuphako pakati pako?

16. Pamenepo akalonga onse a kunyanja adzatsika ku mipando yacifumu yao, nadzabvula zobvala zao zopikapika, nadzabvala kunjenjemera, nadzakhala panthaka pansi, nadzanjenjemera mphindi zonse ndi kukudabwa.

17. Ndipo adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kunena nawe, Watayika bwanji, ndiwe pakhala pa anthu a panyanja, mudzi womveka, unalimbika panyanja, uwo ndi okhalamo, amene anakhalitsa kuopsa kwao pa onse okhala momwemo!

18. Pamenepo zisumbu zidzanjenjemera tsiku la kugwa kwako, inde zisumbu za kunyanja zidzatenga nkhawa pa kucokera kwako.

19. Pakuti atero Ambuye Yehova, Pamene ndikusandutsa mudzi wapasuka, ngati midzi yosakhalamo anthu, ndi kukukweretsera nyanja, nadzakumiza madzi akuru;

20. pamenepo ndidzakutsitsa nao otsikira kumanda, kwa anthu a kale lomwe, ndi kukukhalitsa ku malo a kunsi kwa dziko, kopasukira kale lomwe, pamodzi nao otsikira kumanda, kuti mwa iwe musakhale anthu; ndipo ndidzaika ulemerero m'dziko la amoyo,

21. ndidzakuika woopsa; ndipo sudzaonekanso, cinkana akufunafuna sudzapezekanso konse, ati Ambuye Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 26