Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 25:12-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Atero Ambuye Yehova, Popeza Edomu anacita mobwezera cilango pa nyumba ya Yuda, naparamula kwakukuru pakuibwezera cilango,

13. cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ndidzatambasulira Edomu dzanja langa, ndi kulilikhira munthu ndi nyama, ndi kulisandutsa labwinja; kuyambira ku Temani mpaka Dedani adzagwa ndi lupanga.

14. Ndipo ndidzalibwezera Edomu cilango mwa dzanja la anthu anga Israyeli; ndipo adzacita m'Edomu monga mwa mkwiyo wanga, ndi ukali wanga; motero adzadziwa kubwezera cilango kwanga, ati Ambuye Yehova.

15. Atero Ambuye Yehova, Popeza Afilisti anacita mobwezera cilango nabwezera cilango ndi mtima wopeputsa kuononga, ndi udani wosatha,

16. cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatambasulira Afilisti dzanja langa, ndi kulikha. Akereti, ndi kuononga otsalira mphepete mwa nyanja.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 25