Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 24:3-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo uphere nyumba yopandukayo fanizo, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tereka mphika; uutereke, nuthire madzi m'menemo.

4. Longamo pamodzi ziwalo zace, ziwalo zonse zokoma, mwendo wathako ndi wamwamba; uudzaze ndi mafupa osankhika.

5. Tengako coweta cosankhika, nuikire mafupa mulu wa nkhuni pansi; ubwadamuke, ndi mafupa ace omwe uwaphike m'mwemo.

6. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Tsoka mudzi wokhetsa mwazi, mphika m'mene muli dzimbiri, losaucokera dzimbiri lace; ucotsemo ciwalo ciwalo; sanaugwera maere.

7. Pakuti mwazi wace uli m'kati mwace anauika pathanthwe poyera, sanautsanulira panthaka kuukwirira ndi pfumbi.

8. Pofuna kuutsa ukali, ndi kubwezera cilango, ndaika mwazi wace pathanthwe poyera, kuti usakwiririke.

9. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Tsoka mudzi wokhetsa mwazi, ndidzakulitsa mulu wa nkhuni.

10. Zicuruke nkhuni, kuleza moto, nyama ipse, uwiritse msuzi wace, ubwadamuke, ndi mafupa ace atibuke.

11. Pamenepo uukhazike pa makara ace opanda kanthu m'menemo, kuti utenthe, nuyake mkuwa wace; ndi kuti codetsa cace cisungunuke m'mwemo, kuti dzimbiri lace lithe.

12. Nchito ya mphika ndi yolemetsa, koma dzimbiri lace lalikuru siliucokera, dzimbiri lace liyenera kumoto.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 24