Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 24:23-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndi zilemba zanu zidzakhala pamitu panu, ndi nsapato zanu ku mapazi anu, simudzacita cisoni kapena kulira, koma mudzaonda ndi mphulupulu zanu, ndi kubulirana wina ndi mnzace.

24. Momwemo Ezekieli adzakhala kwa inu cizindikilo; umo monse anacitira iye mudzacita ndinu; cikadza ici mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

25. Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, sikudzakhala kodi tsiku loti ndiwacotsera mphamvu yao, cimwemwe cao copambana, cowakonda m'maso mwao, ndi cokhumbitsa mtima wao, ana ao amuna ndi akazi,

26. kuti tsiku lomwelo wopulumukayo adzakudzera, kukumvetsa m'makutu mwako?

27. Tsiku lomwelo pakamwa pako padzatsegukira wopulumukayo; mudzalankhula osakhalanso cete, momwemo udzawakhalira cizindikilo; ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 24