Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 24:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Anandidzeranso mau a Yehova caka cacisanu ndi cinai, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, ndi kuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, Udzilembere dzina la tsiku lomwe lino, mfumu ya ku Babulo wayandikira Yerusalemu tsiku lomwe lino.

3. Ndipo uphere nyumba yopandukayo fanizo, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tereka mphika; uutereke, nuthire madzi m'menemo.

4. Longamo pamodzi ziwalo zace, ziwalo zonse zokoma, mwendo wathako ndi wamwamba; uudzaze ndi mafupa osankhika.

5. Tengako coweta cosankhika, nuikire mafupa mulu wa nkhuni pansi; ubwadamuke, ndi mafupa ace omwe uwaphike m'mwemo.

6. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Tsoka mudzi wokhetsa mwazi, mphika m'mene muli dzimbiri, losaucokera dzimbiri lace; ucotsemo ciwalo ciwalo; sanaugwera maere.

7. Pakuti mwazi wace uli m'kati mwace anauika pathanthwe poyera, sanautsanulira panthaka kuukwirira ndi pfumbi.

8. Pofuna kuutsa ukali, ndi kubwezera cilango, ndaika mwazi wace pathanthwe poyera, kuti usakwiririke.

9. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Tsoka mudzi wokhetsa mwazi, ndidzakulitsa mulu wa nkhuni.

10. Zicuruke nkhuni, kuleza moto, nyama ipse, uwiritse msuzi wace, ubwadamuke, ndi mafupa ace atibuke.

11. Pamenepo uukhazike pa makara ace opanda kanthu m'menemo, kuti utenthe, nuyake mkuwa wace; ndi kuti codetsa cace cisungunuke m'mwemo, kuti dzimbiri lace lithe.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 24