Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 23:6-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. obvala cibakuwa, ziwanga, ndi akazembe, onsewo anyamata ofunika, anthu oyenda pa akavalo.

7. Ndipo anacita nao zigololo zace, ndiwo anthu osankhika a ku Asuri onsewo, ndipo ali onse anawaumirira anadziipsa nao mafano ao.

8. Sanalekanso zigololo zace zocokera ku Aigupto, pakuti anagona naye m'unamwali wace, nakhudza maere a unamwali wace, namtsanulira cigololo cao.

9. Cifukwa cace ndampereka m'dzanja la mabwenzi ace, m'dzanja la Aasuri amene anawaumirira.

10. Iwowa anabvula umarisece wace, anatenga ana ace amuna ndi akazi, namupha iyeyu ndi lupanga; ndi dzina lace linamveka mwa akazi atamcitira maweruzo.

11. Pamene mng'ono wace Oholiba anaciona, anabvunda ndi kuumirira kwace koposa iyeyo; ndi zigololo zace zidaposa zigololo za mkuru wace.

12. Anaumirira Aasuri, ziwanga, ndi akazembe oyandikizana naye, obvala zangwiro, anthu oyenda pa akavalo, onsewo anyamata ofunika.

13. Ndipo ndinamuona kuti anadetsedwa, onse awiri adatenga njira yomweyi.

14. Ndipo anaonjeza zigololo zace, naona amuna olembedwa pakhoma, zithunzithunzi za Akasidi olembedwa ndi kundwe;

15. omangira malamba m'cuuno mwao, ndi nduwira zazikuru zonika pamitu pao, maonekedwe ao ngati akalonga onsewo, akunga a ku Babulo, dziko la kubadwa kwao ndi Kasidi.

16. Ndipo pakuwaona anawalakalaka, nawatumira mithenga ku dziko la Akasidi.

17. Namdzera a ku Babulo ku kama wa cikondi, namdetsa ndi cigololo cao, iyenso anadetsedwa nao; atatero moyo wace unafukidwa nao.

18. M'mwemo iye anaulula cigololo cace, nabvula umarisece wace; pamenepo moyo wanga unaipidwa naye, monga umo moyo unaipidwira mkuru wace.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 23