Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 23:42-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. Ndipo phokoso lalikuru lidaleka pomwepo, ndipo pamodzi ndi anthu wamba anabwera nao alodzera ocokera kucipululu, naika makoza m'manja mwa awiriwo, ndi akorona okongola pamitu pao.

43. Pamenepo ndinati za uyu anakalamba nazo zigololo, Tsopano iwo adzacita zigololo naye, ndi iyenso nao.

44. Ndipo analowa kwa iye monga umo amalowera kwa mkazi wacigololo, motero analowa kwa Ohola ndi Oholiba akazi oipawo.

45. Ndipo anthu olungama adzawaweruza monga mwa maweruzo a acigololo, ndi maweruzo a akazi okhetsa mwazi; pakuti ndiwo acigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi.

46. Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzawakweretsera msonkhano wa anthu, ndi kuwapereka awazunze, ndi kulanda cuma cao.

47. Ndi msonkhanowo udzawaponya miyala, ndi kuwatha ndi malupanga ao, adzawapha ana ao amuna ndi akazi, ndi kutentha nyumba zao ndi moto.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 23