Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 23:33-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Udzadzala ndi kuledzera ndi cisoni, ndi cikho codabwitsa ndi ca cipasuko, ndi cikho ca mkuru wako Samariya.

34. Udzamwa ici ndi kugugudiza, ndi kuceceta-ceceta zibade zace, ndi kung'amba maere ako; pakuti ndacinena, ati Ambuye Yehova.

35. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza wandiiwala Ine, ndi kunditaya pambuyo pako, uzisenza iwenso coipa cako ndi zigololo zako.

36. Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? uwafotokozere tsono zonyansa zao.

37. Pakuti anacita cigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi, ndipo anacita cigololo ndi mafano ao, nawapititsiranso pamoto ana ao amuna amene anandibalira, kuti athedwe.

38. Anandicitiranso ici, anadetsa malo anga opatulika tsiku lomwelo naipsa masabata anga;

39. pakuti ataphera mafano ao, ana ao analowa tsiku lomwelo m'malo anga opatulika kuwadetsa; ndipo taona, anatero m'kati mwa nyumba yanga.

40. Ndiponso munatuma kuitana anthu ocokera kutali, ndiwo munawatumira mthenga; ndipo taona, anadza amenewo unasamba, cifukwa ca iwo unapaka maso ako mankhwala, ndi kubvala zokometsera;

41. ndipo unakhala pa kama waulemu, pali gome lokonzekeratu patsogolo pace; pamenepo unaika cofukiza conga ndi mafuta anga.

42. Ndipo phokoso lalikuru lidaleka pomwepo, ndipo pamodzi ndi anthu wamba anabwera nao alodzera ocokera kucipululu, naika makoza m'manja mwa awiriwo, ndi akorona okongola pamitu pao.

43. Pamenepo ndinati za uyu anakalamba nazo zigololo, Tsopano iwo adzacita zigololo naye, ndi iyenso nao.

44. Ndipo analowa kwa iye monga umo amalowera kwa mkazi wacigololo, motero analowa kwa Ohola ndi Oholiba akazi oipawo.

45. Ndipo anthu olungama adzawaweruza monga mwa maweruzo a acigololo, ndi maweruzo a akazi okhetsa mwazi; pakuti ndiwo acigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi.

46. Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzawakweretsera msonkhano wa anthu, ndi kuwapereka awazunze, ndi kulanda cuma cao.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 23