Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 23:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, panali akazi awiri, mai wao ndi mmodzi;

3. ndipo anacita cigololo iwo m'Aigupto, anacita cigololo m'ubwana wao; pomwepo anthu anasindikiza maere ao, pomweponso anakhudza nsonga za maere za unamwali wao.

4. Ndipo maina ao ndiwo Ohola wamkuru, ndi Oholiba mng'ono wace; nakhala anga, nabala ana amuna ndi akazi. Ndipo maina ao, Samariya ndiye Ohola, ndi Yerusalemu ndiye Oholiba.

5. Koma Ohola anacita cigololo pamene anali wanga, anaumirira mabwenzi ace Aasuri oyandikizana naye;

6. obvala cibakuwa, ziwanga, ndi akazembe, onsewo anyamata ofunika, anthu oyenda pa akavalo.

7. Ndipo anacita nao zigololo zace, ndiwo anthu osankhika a ku Asuri onsewo, ndipo ali onse anawaumirira anadziipsa nao mafano ao.

8. Sanalekanso zigololo zace zocokera ku Aigupto, pakuti anagona naye m'unamwali wace, nakhudza maere a unamwali wace, namtsanulira cigololo cao.

9. Cifukwa cace ndampereka m'dzanja la mabwenzi ace, m'dzanja la Aasuri amene anawaumirira.

10. Iwowa anabvula umarisece wace, anatenga ana ace amuna ndi akazi, namupha iyeyu ndi lupanga; ndi dzina lace linamveka mwa akazi atamcitira maweruzo.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 23