Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 21:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo kudzakhala akanena ndi iwe, Uusa moyo cifukwa ninji? uzikati, Cifukwa ca mbiri; pakuti ikudza, ndi mtima uli wonse udzasungunuka, ndi manja onse adzalenda, ndi mzimu uli wonse udzakomoka, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi; taona irinkudza, inde idzacitika, ati Ambuye Yehova.

8. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

9. Wobadwa ndi munthu iwe, nenera ndi kuti, Atero Yehova, Nena, Lupanga, lupanga lanoledwa, latuulidwanso;

10. lanoledwa kuti liphetu, lituulidwa kuti linge mphezi; tisekererepo kodi? ndilo ndodo yacifumu ya mwana wanga, yopeputsa mtengo uli wonse.

11. Ndipo analipereka alituule, kuti acite nalo lupangali analinola, inde analituula kulipereka m'dzanja la wakupha.

12. Pfuula ndi kulira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti likhalira pa anthu anga, likhalira pa akalonga onse a Israyeli, laperekedwa kulupanga pamodzi ndi anthu anga; cifukwa cace panda pancafu pako.

13. Pakuti pali kuyesedwa; ndipo nanga ndodo yacifumu yopeputsa ikapanda kukhalanso? ati Ambuye Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 21