Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 19:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Mai wako ananga mpesa wookedwa kumadzi; muja anakhala mumtendere unabala zipatso, wodzala ndi nthambi, cifukwa ca madzi ambiri.

11. Ndipo unali nazo ndodo zolimba zikhale ndodo zacifumu, za ocita ufumu, ndi msinkhu wao unakula kufikira kumitambo, nizinaoneka m'kusomphoka kwao pakati pa nthambi zace zambiri.

12. Koma unazulidwa mwaukali, unaponyedwa pansi ndi mphepo ya kum'mawa, inaumitsa zipatso zace, ndodo zace zolimba zinatyoka ndi kuuma, moto unazitha.

13. Ndipo tsopano waokedwa m'cipululu m'dziko louma ndi la ludzu.

14. Unaturukanso moto ku ndodo za ku nthambi zace, unatha zipatso zace; m'mwemo ulibe ndodo yolimba ikhale ndodo yacifumu ya kucita ufumu. Iyi ndi nyimbo idzakhala nyimbo ya maliro.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 19