Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 18:5-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Koma munthu akakhala wolungama, nakacita ciweruzo ndi cilungamo,

6. wosadya pamapiripo, wosakweza maso ace ku mafano a nyumba ya Israyeli, wosaipsa mkazi wa mnansi wace, kapena kuyandikira mkazi ataoloka,

7. wosasautsa munthu ali yense, koma wambwezera wangongole cigwiriro cace, wosatenga zofunkha, anampatsa wanjala cakudya cace, nabveka wamarisece ndi cobvala,

8. wosapereka molira phindu, wosatenga coonjezerapo wobweza dzanja lace lisacite cosalungama, woweruza zoona pakati pa munthu ndi mnzace,

9. amayenda m'malemba anga, nasunga maweruzo anga kucita cokhulupirika; iye ndiye wolungama, adzakhala ndi moyo ndithu, anena Ambuye Yehova.

10. Akabala mwana ndiye mkhungu, wokhetsa mwazi, wocita cimodzi ca izi,

11. wosacita zabwino zonse zija, koma anadyanso pamapiri, naipsa mkazi wa mnansi wace,

12. nasautsa osauka ndi osowa, natenga zofunkha, wosabwezera cigwiriro, nakweza maso ace kumafano, nacita conyansa,

13. napereka molira phindu, nalandira coonjezerapo; adzakhala ndi moyo uyu kodi? sadzakhala ndi moyo, anacita zonyansa izi zonse; kufa adzafadi, niwazi wace umkhalira.

14. Taona tsono, yemweyo akabala mwana uyu, naona zocimwa zonse adazicita atate wace, naopa wosacita zoterezo,

15. wosadya pamapiri, kapena kukweza maso ace ku mafano a nyumba ya Israyeli, wosaipsa mkazi wa mnansi wace,

16. kapena kusautsa wina ali yense, wosatenga cigwiriro, wosatenga zofunkha; koma anapatsa wanjala cakudya cace, nabveka wamarisece ndi cobvala,

17. naletsa dzanja lace pa wozunzika, wosalandira phindu kapena coonjezerapo, wocita maweruzo anga, nayenda m'malemba anga; uyu sadzafera mphulupulu ya atate wace, adzakhala ndi moyo ndithu.

18. Atate wace, popeza anazunza cizunzire, nafunkha za mbale wace, nacita cimene siciri cabwino pakati pa anthu ace, taona, adzafa mu mphulupulu yace.

19. Koma inu mukuti, Alekeranji mwana kusenza mphulupulu za atate wace? Mwanayo akacita ciweruzo ndi cilungamo, nakasunga malemba anga onse, ndi kuwacita, adzakhala ndi moyo ndithu.

20. Moyo wocimwawo ndiwo udzafa; mwana sadzasenza mphulupulu zaatate wace, ndi atate sadzasenza mphulupulu za mwana; cilungamo ca wolungama cidzamkhalira, ndi coipa ca woipa cidzamkhalira,

21. Koma woipayo akabwerera kusiya macimo ace onse adawacita nakasunga malemba anga onse, ndi kucita ciweruzo ndi cilungamo, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.

22. Nnena cimodzi conse ca zolakwa zace zonse adazicita cidzakumbukika cimtsutse; m'cilungamo cace adacicita adakhala ndi moyo.

23. Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yace, ndi kukhala ndi moyo?

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 18