Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 18:19-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Koma inu mukuti, Alekeranji mwana kusenza mphulupulu za atate wace? Mwanayo akacita ciweruzo ndi cilungamo, nakasunga malemba anga onse, ndi kuwacita, adzakhala ndi moyo ndithu.

20. Moyo wocimwawo ndiwo udzafa; mwana sadzasenza mphulupulu zaatate wace, ndi atate sadzasenza mphulupulu za mwana; cilungamo ca wolungama cidzamkhalira, ndi coipa ca woipa cidzamkhalira,

21. Koma woipayo akabwerera kusiya macimo ace onse adawacita nakasunga malemba anga onse, ndi kucita ciweruzo ndi cilungamo, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.

22. Nnena cimodzi conse ca zolakwa zace zonse adazicita cidzakumbukika cimtsutse; m'cilungamo cace adacicita adakhala ndi moyo.

23. Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yace, ndi kukhala ndi moyo?

24. Koma wolungamayo akabwerera kuleka cilungamo cace, nakacita mphulupulu, ndi kucita monga mwa zonyansa zonse azicita woipa, adzakhala ndi moyo kodi? Nnena cimodzi ca zolungama zace zonse adzazicita cidzakumbukika m'kulakwa kwace analakwa nako, ndi m'kucimwa kwace anacimwa nako; momwemo adzafa.

25. Koma mukuti, Njira ya Ambuye njosayenera. Tamvera tsono nyumba ya Israyeli, Kodi njira yanga njosayenera? njira zanu si ndizo zosayenera?

26. Wolungamayo akatembenukira kuleka cilungamo cace, nakacita mphulupulu, adzafa momwemo; m'mphulupulu yace adaicita adzafa.

27. Ndipo woipayo akatembenukira kuleka coipa cace adacicita, nakacita ciweruzo ndi cilungamo, adzapulumutsa moyo wace.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 18