Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 17:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ciombankhanga cacikuru ndi mapiko akuru, ndi maphiphi atali, odzala nthenga ca mathotho-mathotho, cinafika ku Lebano, nicitenga nsonga ya mkungudza,

4. cinabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zace zanthete, ndi kumuka nayo ku dziko la malonda, cinaiika m'mudzi wa amalonda.

5. Cinatengakonso mbeu ya m'dziko, ndi kuibzala m'nthaka yokoma, cinaiika panali madzi ambiri, cinaioka ngati mtengo wamsondodzi.

6. Ndipo inaphuka, nikhala mpesa wotambalala wofupi msinkhu, nthambi zace zinapindikira momwe, ndi mizu yace pansi pace, nikhala mpesa, nuonetsa nthambi ndi kuphuka mphukira.

7. Panalinso ciombankhanga cina cacikuru, ndi mapiko akuru, ndi nthenga zambiri; ndipo taona, mpesa uwu unacipindira mizu yace, nucilunjikitsira nthambi zace, kucokera pookedwa pace, kuti ciuthirire madzi.

8. Unaokedwa mu nthaka yabwino kuli madzi ambiri, kuti uphuke nthambi, nubale zipatso, nukhale mpesa wabwino.

9. Uziti, Atero Ambuye Yehova, Udzakondwa kodi? sadzausula ndi kudula zipatso zace, kuti uume, kuti masamba ace onse ophuka aume, ngakhale palibe mphamvu yaikuru, kapena anthu ambiri akuuzula?

10. Inde ungakhale waokedwa udzakondwa kodi? sudzauma ciumire kodi pakuuomba mphepo ya kum'mawa? udzauma pookedwa apo udaphuka.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 17