Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 17:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, ipha mwambi, nunene fanizo kwa nyumba ya Israyeli,

3. nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ciombankhanga cacikuru ndi mapiko akuru, ndi maphiphi atali, odzala nthenga ca mathotho-mathotho, cinafika ku Lebano, nicitenga nsonga ya mkungudza,

4. cinabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zace zanthete, ndi kumuka nayo ku dziko la malonda, cinaiika m'mudzi wa amalonda.

5. Cinatengakonso mbeu ya m'dziko, ndi kuibzala m'nthaka yokoma, cinaiika panali madzi ambiri, cinaioka ngati mtengo wamsondodzi.

6. Ndipo inaphuka, nikhala mpesa wotambalala wofupi msinkhu, nthambi zace zinapindikira momwe, ndi mizu yace pansi pace, nikhala mpesa, nuonetsa nthambi ndi kuphuka mphukira.

7. Panalinso ciombankhanga cina cacikuru, ndi mapiko akuru, ndi nthenga zambiri; ndipo taona, mpesa uwu unacipindira mizu yace, nucilunjikitsira nthambi zace, kucokera pookedwa pace, kuti ciuthirire madzi.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 17