Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 16:6-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo popita Ine panali iwepo, ndinakuona ulikubvimvinizika m'mwazi wako. Pamenepo ndinanena ndi iwe m'mwazi wako, Khala ndi moyo, inde ndinati kwa iwe m'mwazi mwako, Khala ndi moyo.

7. Ndinakucurukitsa ngati mphundu za kumunda; ndipo unathululuka ndi kukula kufikira wakongola nkhope, maere ako anamera, ndi tsitsi lako linamera; koma unali wamarisece ndi wausiwa.

8. Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakupfunda copfunda canga, ndi kuphimba umarisece wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.

9. Ndipo ndinakusambitsa ndi madzi, inde ndinakutsuka kukucotsera mwazi wako, ndi kukudzoza mafuta.

10. Ndinakubvekanso ndi nsaru zopikapika, ndi kukubveka nsapato za cikopa ca katumbu; ndinakuzenenga nsaru yabafuta, ndi kukuphimba ndi nsaru yasilika.

11. Ndinakukometseranso ndi zokometsera, ndi kuika zigwinjiri m'manja mwako, ndi unyolo m'khosi mwako.

12. Momwemo ndinaika cipini m'mphuno mwako, ndi maperere m'makutu mwako, ndi korona wokongola pamutu pako.

13. Ndipo unadzikometsera ndi golidi, ndi siliva, ndi cobvala cako ndi bafuta ndi silika ndi yopikapika; unadya ufa wosalala, ndi uci, ndi mafuta; ndipo unali wokongola woposa ndithu, ndipo unapindula-pindula kufikira unasanduka ufumu.

14. Ndi mbiri yako inabuka mwa amitundu cifukwa ca kukongola kwako; pakuti ndiko kwangwiro, mwa ulemerero wanga ndinauika pa iwe, ati Ambuye Yehova.

15. Koma unatama kukongola kwako, ndi kucita zacigololo potama mbiri yako, ndi kutsanulira zigololo zako pa munthu ali yense wopitapo; unali wace.

16. Ndipo unatengako zobvala zako, ndi kudzimangira misanje ya mawanga mawanga, ndi kucitapo cigololo; zotere sizinayenera kufika kapena kucitika.

17. Unatenganso zokometsera zako zokoma za golidi wanga ndi siliva wanga, zimene ndinakupatsa, ndi kudzipangira mafano a amuna, ndi kucita nao cigololo.

18. Unatenganso zobvala zako za nsaru yopikapika, ndi kuwabveka nazo, unaikanso mafuta anga ndi cofukiza canga pamaso pao.

19. Ndi mkate wanga ndinakupatsawo, ufa wosalala, ndi mafuta, ndi uci, ndinakudyetsazo, unawaikira izi pamaso pao, zicite pfungo lokoma; kunatero, ati Ambuye Yehova.

20. Unatenganso ana ako amuna ndi akazi amene unandibalirawo, ndi kuwapereka nsembe awathe. Zigololo zako zidacepa kodi,

21. kuti unawapha ana anga ndi kuwapereka, pakuwapititsa pamoto?

22. Ndipo pa zonyansa zako zonse ndi zigololo zako sunakumbukila masiku a ubwana wako, mujaunakhala wamarisece ndi wausiwa, wobvimvinizika m'mwazi wako.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 16