Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 16:51-58 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

51. Ngakhale Samariya sanacita theka la zocimwa zako, koma unacurukitsa zonyansa zako kuwaposa iwowa, ndi kuika abale ako olungama ndi zonyansa zako zonse unazicita.

52. Usenzenso manyazi ako, iwe wakuweruza abale ako mwa zocimwa zako unazicita monyansa koposa iwowa; iwo akuposa iwe m'cilungamo cao, nawenso ucite manyazi nusenze manyazi ako, popeza waika abale ako olungama.

53. Ndipo ndidzabweza undende wao, undende wa Sodomu ndi ana ace, ndi undende wa Samariya ndi ana ace, ndi undede wa andende ako pakati pao;

54. kuti usenze manyazi ako, ndi kuti ucite manyazi cifukwa ca zonse unazicita pakuwatonthoza.

55. Ndipo abale ako Sodomu ndi ana ace adzabwerera umo unakhalira kale; ndi iwe ndi ana ako mudzabwerera umo munakhalira kale.

56. Ndipo sunakamba za mbale wako Sodomu pakamwa pako tsiku la kudzikuza kwako;

57. cisanabvundukuke coipa cako monga nthawi ya citonzo ca ana akazi a Aramu, ndi onse akumzungulira iye, ana akazi a Afilisti akupeputsa pozungulira ponse.

58. Wasenza coipa cako ndi zonyansa zako, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 16