Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 14:11-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. kuti nyumba ya Israyeli isasocerenso kusatsata Ine, kapena kudzidetsanso ndi zolakwa zao zonse; koma kuti akhale anthu anga, ndipo ndikhale Ine Mulungu wao, ati Ambuye Yehova.

12. Ndipo anandidzera mau a Yehova akuti,

13. Likandicimwira dziko ndi kucita monyenga, ndipo ndikalitambasulira dzanja langa, ndi kulityolera mcirikizo wace, ndiwo mkate, ndi kulitumizira njala, ndi kulidulira munthu ndi nyama,

14. cinkana akadakhala m'mwemo anthu awa atatu, Nowa, Danieli, ndi Yobu, akadapulumutsa moyo wao wokha mwa cilungamo cao, ati Ambuye Yehova.

15. Ndikapititsa zirombo zoipa pakati pa dziko, nizipulula ana, kuti likhale lacipululu losapitako munthu cifukwa ca zirombo,

16. cinkana anthu omwewo atatu akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; iwo akadapulumuka okha; koma dziko likadakhala lacipululu.

17. Kapena ndikadza pa dziko ndi lupanga, ndi kuti, Lupanga lipite pakati pa dziko, kuti ndilidulire munthu ndi nyama;

18. cinkana anthu atatuwo akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; koma iwo akadapulumuka okha.

19. Kapena ndikatumizira dzikolo mliri, ndi kulitsanulira ukali wanga ndi mwazi, kulidulira munthu ndi nyama;

20. cinkana Nowa, Danieli, ndi Yobu, akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; akadapulumutsa moyo wao wokha ndi cilungamo cao.

21. Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zirombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama?

22. Koma onani mudzatsala opulumuka m'mwemo amene adzaturutsidwa, ndiwo ana amuna ndi akazi; taonani, adzaturuka kudza kwa inu; ndipo mudzaona njira zao, ndi zocita zao; mudzatonthozedwanso pa zoipa ndazitengera pa Yerusalemu, inde pa zonse ndazitengerapo.

23. Ndipo adzakusangalatsani pamene muona njira yao, ndi zocita zao; ndipo mudzadziwa kuti sindinazicita kopanda cifukwa zonse ndinazicita momwemo, ati Ambuye Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 14