Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 14:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo anafika kwa ine akulu ena a Israyeli nakhala pansi pamaso panga.

2. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

3. Wobadwa ndi munthu iwe, anthu awa anautsa mafano ao mumtima mwao, naimika cokhumudwitsa ca mphulupulu yao pamaso pao; ndifunsidwe nao konse kodi?

4. Cifukwa cace ulankhule nao, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Ali yense wa nyumba ya Israyeli wakuutsa mafano ace mumtima mwace, naimika cokhumudwitsa ca mphulupulu yace pamaso pace, nadza kwa mneneri, Ine Yehova ndidzamyankhapo monga mwa mafano ace aunyinji;

5. kuti ndigwire nyumba ya Israyeli mumtima mwao; popeza onsewo asanduka alendo ndi Ine mwa mafano ao.

6. Cifukwa cace uziti kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Bwerani, lekani mafano anu, tembenuzani nkhope zanu kuzisiya zonyansa zanu zonse.

7. Pakuti ali yense wa nyumba ya Israyeli, kapena wa alendo ogonera m'Israyeli, wodzisiyanitsa kusatsata Ine, nautsa mafano ace m'mtima mwace, naimika cokhumudwitsa ca mphulupulu yace pamaso pace, nadzera mneneri kudzifunsira kwa Ine, Ine Yehova ndidzamyankha ndekha;

8. ndipo ndidzaikira munthu uyu nkhope yanga imtsutse, ndi kumuyesa codabwitsa, ndi cizindikilo, ndi mwambi, ndi kumsadza pakati pa anthu anga; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

9. Ndipo akaceteka mneneriyo, nakanena mau, Ine Yehova ndamceta mneneri uja; ndipo ndidzamtambasulira dzanja langa, ndi kumuononga pakati pa anthu anga Israyeli.

10. Ndipo adzasenza mphulupulu yao, mphulupulu ya mneneri idzanga mphulupulu ya uja wamfunsira;

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 14