Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 12:20-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndi midzi yokhalamo anthu idzapasuka, ndi dziko lidzakhala labwinja; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

21. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

22. Wobadwa ndi munthu iwe, ngwotani mwambi umene muli nao m'dziko la Israyeli, wakuti, Masiku acuruka, ndi masomphenya ali onse apita pacabe?

23. Cifukwa cace unene nao, Atero Yehova Mulungu, Ndidzaleketsa mwambi uwu, ndipo sadzauchulanso mwambi m'Israyeli; koma unene nao, Masiku ayandikira, nadzacitika masomphenya ali onse.

24. Pakuti sikudzakhalanso masomphenya acabe, kapena ula wosyasyalika m'nyumba ya Israyeli.

25. Pakuti Ine ndine Yehova, ndidzanena, ndi mau ndidzanenawo adzacitika, osazengerezekanso; pakuti m'masiku anu, nyumba yopanduka inu, ndidzanena mau ndi kuwacita, ati Yehova Mulungu.

26. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

27. Wobadwa ndi munthu iwe, taona, iwo a nyumba ya Israyeli akuti, masomphenya awaona ndiwo a masiku ambiri: ndipo anenera za nthawi ziri kutali,

28. Cifukwa cace uziti nao, Atero Ambuye Yehova, Palibe amodzi a mau anga adzazengerezekanso; koma mau ndidzanenawo adzacitika, ati Ambuye Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 12