Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 11:2-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, awa ndi anthu olingirira za mphulupulu, ndi kupangira uphungu woipa m'mudzi muno;

3. ndiwo akuti, siinafike nyengo yakumanga nyumba; mudzi uwu ndi mphika, ife ndife nyama.

4. Cifukwa cace uwanenere, neneratu, wobadwa ndi munthu iwe.

5. Pamenepo mzimu wa Yehova unandigwera, ndipo ananti kwa ine, Nena, Atero Yehova, Mwatero nyumba ya Israyeli, pakuti ndidziwa zimene zimalowa m'mtima mwanu.

6. Mwacurukitsa ophedwa anu m'mudzi muno, mwadzazanso makwalala ace ndi ophedwawo.

7. Cifukwa cace atero Yehova Mulungu, Ophedwa anu munawaika m'kati mwace, iwo ndiwo nyama imene, ndi mudzi uwu ndiwo mphika; koma inu mudzaturutsidwa m'kati mwace.

8. Mwaopa lupanga, tsono ndidzakufikitsirani lupanga, ati Yehova Mulungu.

9. Ndipo ndidzakuturutsani m'kati mwace, ndi kukuperekani m'manja a alendo, ndi kucita maweruzo pakati panu.

10. Mudzagwa ndi lupanga, ndidzakuweruzirani ku malire a Israyeli; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

11. Mudzi uno sudzakhala mphika wanu, ndi inu simudzakhala nyama m'kati mwace, ndidzakuweruzirani ku malire a Israyeli;

12. ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuti simunayenda m'malemba anga, kapena kucita maweruzo anga, koma mwacita monga mwa maweruzo a amitundu okhala pozungulira panu.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 11