Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 11:18-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo adzafikako, nadzacotsako zonyansa zace zonse, ndi zace zonse zakuipitsamo.

19. Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawacotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;

20. kuti ayende m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwacita; ndipo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.

21. Koma iwo amene mtima wao unatsata mtima wa zonyansa zao, ndi zoipitsitsa zao, ndidzawabwezera njira yao pamtu pao, ati Yehova Mulungu.

22. Pamenepo akerubi anatambasula mapiko ao, ndi njinga zinali pa mbali pao; ndi ulemerero wa Mulungu wa Israyeli unali pamwamba pao.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 11