Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 10:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo panaoneka pa akerubi conga dzanja la munthu pansi pa mapiko ao.

9. Pamenepo ndinapenya, ndipo taonani, njinga zinai m'mbali mwa akerubi, njinga imodzi m'mbali mwa kerubi mmodzi, ndi njinga yina m'mbali mwa kerubi wina, ndi maonekedwe a njingazi ananga mawalidwe a berulo.

10. Ndipo maonekedwe ace, zonse zinai zinafanana, ngati njinga ziwiri zopingasitsana,

11. Pakuyenda akerubi anayenda ku mbali zao zinai, sanatembenuka poyenda; koma komwe udalozako mutu anatsatako, sanatembenuka poyenda.

12. Ndipo thupi lao lonse, ndi misana yao, ndi manja ao, ndi mapiko ao, ndi njinga zomwe, zinadzala ndi maso pozungulira pao, zingakhale njingazi anai aja anali nazo.

13. Kunena za njingazi, wina anazipfuulira, ndiri cimvere ine, Kunkhulirani.

14. Ndipo ali yense anali nazo nkhope zinai, nkhope yoyamba ndiyo nkhope ya kerubi, ndi nkhope yaciwiri ndiyo nkhope ya munthu, ndi yacitatu ndiyo nkhope ya mkango, ndi yacinai ndiyo nkhope ya ciombankhanga.

15. Pamenepo akerubi anakwera, ndizo zamoyo zija ndinaziona kumtsinje Kebara.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 10