Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 10:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, ku thambo lokhala pamwamba pa mitu ya akerubi kudaoneka ngati mwala wasafiro, ngati maonekedwe a cifaniziro ca mpando wacifumu pamwamba pao.

2. Ndipo Yehova analankhula ndi munthu wobvala bafuta, nati, Lowa pakati pa njingazi pansi pa kerubi, nudzaze manja ako makara a moto ocokera pakati pa akerubi, nuwamwaze pamwamba pa mudzi. Nalowa, ndiri cipenyere ine.

3. Tsono akerubi anaima ku dzanja lamanja la nyumba polowa munthuyo, ndi mtambo unadzara bwalo la m'kati.

4. Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kucokera kukerubi kumka ku ciundo ca nyumba; ndi nyumba inadzala nao mtambo, ndi bwalo linadzala ndi ceza ca ulemerero wa Yehova.

5. Ndipo mkokomo wa mapiko a akerubi unamveka mpaka bwalo lakunja, ngati mau a Mulungu Wamphamvuyonse, pakunena Iye.

6. Ndipo kunali pomlamulira munthu wobvala bafutayo, ndi kuti, Para moto pakati pa njingazi ndi pakati pa akerubi; iye analowa, naima m'mbali mwa njinga.

7. Pamenepo kerubi wina anatambasula dzanja lace pakati pa akerubi ku moto uli pakati pa akerubi, naparako, nauika m'manja mwa iye wobvala bafuta, ndiye naulandita, naturuka.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 10