Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kucokera kukerubi kumka ku ciundo ca nyumba; ndi nyumba inadzala nao mtambo, ndi bwalo linadzala ndi ceza ca ulemerero wa Yehova.