Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 2:61-70 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

61. Ndi ana a ansembe: ana a Habaya, ana a Kozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgileadi, nachedwa dzina lao.

62. Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa cibadwidwe cao, koma osawapeza; potero anacotsedwa ku nchito ya nsembe monga odetsedwa.

63. Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulikitsa, mpaka adzabuka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu.

64. Msonkhano wonse pamodzi ndiwo wa zikwi makumi anai ndi awiri mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi,

65. osawerenga akapolo ao amuna ndi akazi, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana atatu ndi makumi atatu kudza asanu ndi awiri; ndipo anakhala nao amuna ndi akazi oyimbira mazana awiri.

66. Akavalo ao ndiwo mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu kudza asanu ndi mmodzi; nyuru zao mazana awiri mphambu makumi anai kudza zisanu;

67. ngamira zao mazana anai mphambu makumi atatu kudza asanu; aburu zikwi zisanu ndi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi awiri.

68. Ndipo akulu ena a nyumba za makolo, pofika ku nyumba ya Yehova iri ku Yerusalemu, anapereka caufulu kwa nyumba ya Mulungu cakulimika pakuzika pace.

69. Monga momwe anakhoza anapereka ku cuma ca nchitoyi madariki agolidi: zikwi zisanu ndi cimodzi, miyeso ya siliva zikwi zisanu, ndi maraya a ansembe zana limodzi.

70. Ndipo ansembe, ndi Alevi, ndi anthu ena, ndi oyimbira, ndi odikira, ndi Anetini, anakhala m'midzi mwao, ndi Aisrayeli onse m'midzi mwao.

Werengani mutu wathunthu Ezara 2