Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 10:17-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Natsiriza nao amuna onse adadzitengera akazi acilendo tsiku loyamba la mwezi woyamba.

18. Ndipo anapeza mwa ana a ansembe odzitengera akazi acilendo, ndiwo a ana a Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ace Maseya, ndi Eliezere, ndi Yaribu, ndi Gedaliya.

19. Ndipo anaimika dzanja lao kuti adzacotsa akazi ao; ndipo popeza adaparamuladi, anapereka nsembe nkhosa yamphongo ya zoweta pa kuparamula kwao.

20. Ndi a ana a Imeri: Hanani ndi Zebadiya.

21. Ndi a ana a Harimu: Maseya, ndi Eliya, ndi Semaya, ndi Yehiyeli, ndi Uziya.

22. Ndi a ana a Pasuru: Elioenai, Maseya, Ismayeli, Netaneli, Yozabadi, ndi. Elasa.

23. Ndi a Alevi: Yozabadi, ndi Simei, ndi Kelaya (ndiye Kelita), Petahiya, Yuda, ndi Eliezere.

24. Ndi a oyimbira: Eliasibu; ndi a odikira: Salumu, ndi Telemu, ndi Uri.

Werengani mutu wathunthu Ezara 10