Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 1:4-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo ali yense wotsala pamalo pali ponse agonerapo iye, anthu a kumalo kwace amthandize ndi siliva, ndi golidi, ndi zoweta, ndi cuma, pamodzi ndi nsembe yaufulu ya kwa nyumba ya Mulungu iri ku Yerusalemu.

5. Pamenepo ananyamuka akulu a nyumba za makolo a Yuda ndi Benjamini, ndi ansembe, ndi Alevi, ndiwo onse amene Mulungu adawautsira mzimu wao akwere kukamanga nyumba ya Yehova iri ku Yerusalemu.

6. Ndipo onse akuwazinga analimbitsa manja ao ndi zipangizo za siliva, ndi golidi, ndi cuma, ndi zoweta, ndi zinthu za mtengo wace, pamodzi ndi nsembe zaufulu.

7. Koresi mfumu anaturutsanso zipangizo za nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara adaziturutsa m'Yerusalemu, ndi kuziika m'nyumba ya milungu yace;

8. zomwezi Koresi mfumu ya ku Perisiya anaziturutsa ndi dzanja la Miteridati wosunga cumayo, naziwerengera Sezibazara kalonga wa Ayuda.

9. Kuwerenga kwace ndiko: mbizi zagolidi makumi atatu, mbizi zasiliva cikwi cimodzi, mipeni makumi awiri mphambu isanu ndi inai;

10. zikho zagolidi makumi atatu, zikho zasiliva zina mazana anai ndi khumi, zipangizo zina cikwi cimodzi.

11. Zipangizo zonse zagolidi ndi zasiliva ndizo zikwi zisanu ndi mazana anai. Izi zonse Sezibazara anakwera nazo, pokwera andende aja kucokera ku Babulo kumka ku Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu Ezara 1