Pamenepo ananyamuka akulu a nyumba za makolo a Yuda ndi Benjamini, ndi ansembe, ndi Alevi, ndiwo onse amene Mulungu adawautsira mzimu wao akwere kukamanga nyumba ya Yehova iri ku Yerusalemu.