Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 9:7-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Napha Parisandata, ndi Dalifoni, ndi Asipata,

8. ndi Porata, ndi Adaliya, ndi Aridata,

9. ndi Parimasta, ndi Arisai, ndi Aridai, ndi Vaisata,

10. ana amuna khumi a Hamani mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalanda zofunkha.

11. Tsiku lomwelo anabwera naco kwa mfumu ciwerengo ca iwo ophedwa m'cinyumba ca ku Susani.

12. Ndipo mfumu inati kwa mkazi wamkuru Estere, Ayuda adapha, naononga amuna mazana asanu m'cinyumba ca ku Susani, ndi ana amuna khumi a Hamani; nanga m'maiko ena a mfumu munacitikanji? pempho lanu ndi ciani tsono? lidzacitikira inu; kapena mufunanjinso? kudzacitika.

13. Nati Estere, Cikakomera mfumu, alole Ayuda okhala m'Susani acite ndi mawa lomwe monga mwa lamulo la lero; ndi ana amuna khumi a Hamani apacikidwe pamtengo.

14. Ndipo mfumu inati azicita motero, nalamulira m'Susani, napacikidwa ana amuna khumi a Hamani.

15. Ndipo Ayuda okhala m'Susani anasonkhana pamodzi, tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi wa Adara, napha amuna mazana atatu m'Susani; koma sanalanda zofunkha.

16. Nasonkhana pamodzi Ayuda ena okhala m'maiko a mfumu, nalimbikira moyo wao, napumula pa adani ao, nawapha a iwo odana nao zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu; koma sanalanda zofunkha.

17. Cinacitika ici tsiku lakhumi ndi citatu la mwezi wa Adara, ndi tsiku lace lakhumi ndi cinai anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwesa.

18. Koma Ayuda okhala m'Susani anasonkhana tsiku lace lakhumi ndi citatu ndi lakhumi ndi cinai, ndi pa tsiku lakhumi ndi cisanu anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwera.

19. Cifukwa cace Ayuda a kumiraga, okhala m'midzi yopanda malinga, amaliyesa tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi wa Adara tsiku la kukondwera ndi madyerero, ndi tsiku lokoma, ndi lakutumizirana magawo.

20. Ndipo Moredekai analembera izi, natumiza akalata kwa Ayuda onse okhala m'maiko onse a mfumu Ahaswero, a kufupi ndi a kutali,

21. kuwalimbikitsira, asunge tsiku lakhumi ndi cinai, mwezi wa Adara, ndi tsiku lace lakhumi ndi cisanu lomwe, caka ndi caka,

22. ndiwo masiku amene Ayuda anapumula pa adani ao; ndi mwezi wacisoni unawasandulikira wakukondwera, ndi wamaliro ukhale tsiku lokoma, awayese masiku amadyerero ndi akukondwera, akutumizirana magawo, ndi akupatsa zaufulu kwa osauka.

Werengani mutu wathunthu Estere 9