Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 9:16-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Nasonkhana pamodzi Ayuda ena okhala m'maiko a mfumu, nalimbikira moyo wao, napumula pa adani ao, nawapha a iwo odana nao zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu; koma sanalanda zofunkha.

17. Cinacitika ici tsiku lakhumi ndi citatu la mwezi wa Adara, ndi tsiku lace lakhumi ndi cinai anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwesa.

18. Koma Ayuda okhala m'Susani anasonkhana tsiku lace lakhumi ndi citatu ndi lakhumi ndi cinai, ndi pa tsiku lakhumi ndi cisanu anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwera.

19. Cifukwa cace Ayuda a kumiraga, okhala m'midzi yopanda malinga, amaliyesa tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi wa Adara tsiku la kukondwera ndi madyerero, ndi tsiku lokoma, ndi lakutumizirana magawo.

20. Ndipo Moredekai analembera izi, natumiza akalata kwa Ayuda onse okhala m'maiko onse a mfumu Ahaswero, a kufupi ndi a kutali,

21. kuwalimbikitsira, asunge tsiku lakhumi ndi cinai, mwezi wa Adara, ndi tsiku lace lakhumi ndi cisanu lomwe, caka ndi caka,

22. ndiwo masiku amene Ayuda anapumula pa adani ao; ndi mwezi wacisoni unawasandulikira wakukondwera, ndi wamaliro ukhale tsiku lokoma, awayese masiku amadyerero ndi akukondwera, akutumizirana magawo, ndi akupatsa zaufulu kwa osauka.

23. Ndipo Ayuda anabvomereza kucita monga umo adayambira, ndi umo Moredekai adawalembera;

24. popeza Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, mdani wa Ayuda onse, adapangira Ayuda ciwembu kuwaononga, naombeza Puri, ndiwo ula, kuwatha ndi kuwaononga;

25. koma pofika mlanduwo kwa mfumu, anati mwa akalata kuti ciwembu cace coipa adacipangira Ayuda, cimbwerere mwini; ndi kuti Iye ndi ana amuna ace apacikidwe pamtengo,

Werengani mutu wathunthu Estere 9