Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 8:12-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. tsiku lomwelo, m'maiko onse a mfumu Ahaswero, tsiku lakhumi ndi citatu la mwezi wakhumi ndi ciwiri, ndiwo mwezi wa Adara.

13. Citsanzo cace, ca lemboli, cakuti abukitse lamulo m'maiko onse, cinalalikidwa kwa mitundu yonse ya anthu, kuti, Ayuda akonzekeretu tsiku lijalo, kubwezera cilango adani ao.

14. Naturuka amtokoma okwera pa akavalo aliwiro acifumu; pakuti mau a mfumu anawafulumiza ndi kuwaumiriza; ndipo lamulolo linabukitsidwa m'cinyumba ca ku Susani.

15. Ndipo Moredekai anaturuka pamaso pa mfumu wobvala cobvala cacifumu camadzi ndi coyera, ndi korona wamkuru wagolidi, ndi maraya abafuta ndi ofiirira; ndi mudzi wa Susani unapfuula ndi kukondwera.

16. Ayuda anali nako kuunika, ndi kukondwera, ndi cimwemwe, ndi ulemu.

17. Ndi m'maiko monse, ndi m'midzi yonse, mudafika mau a mfumu ndi lamulo lace, Ayuda anali nako kukondwera ndi cimwemwe, madyerero ndi tsiku lokoma. Ndipo ambiri a mitundu ya anthu a m'dziko anasanduka Ayuda; pakuti kuopsa kwa Ayuda kudawagwera.

Werengani mutu wathunthu Estere 8