Ndi m'maiko monse, ndi m'midzi yonse, mudafika mau a mfumu ndi lamulo lace, Ayuda anali nako kukondwera ndi cimwemwe, madyerero ndi tsiku lokoma. Ndipo ambiri a mitundu ya anthu a m'dziko anasanduka Ayuda; pakuti kuopsa kwa Ayuda kudawagwera.